9 Wansembeyo anayankha kuti: “Limene lilipo ndi lupanga la Goliyati+ Mfilisiti amene unamupha mʼchigwa cha Ela.+ Lakulungidwa ndi nsalu ndipo lili kuseli kwa efodi.+ Ngati ungalikonde ukhoza kutenga, chifukwa lilipo ndi lokhalo.” Ndiyeno Davide anati: “Palibenso lina ngati limeneli, ndipatseni.”