13 Nthawi yomweyo Davide anauza amuna amene anali naye kuti: “Aliyense amangirire lupanga lake mʼchiuno!”+ Choncho onse anamangirira malupanga awo mʼchiuno ndipo Davide nayenso anamangirira lake. Amuna pafupifupi 400 anapita limodzi ndi Davide, koma 200 anatsala kuti aziyangʼanira katundu.