6 Davide anali ndi nkhawa kwambiri chifukwa anthu ankakambirana zoti amuponye miyala. Anthuwo ankafuna kuchita zimenezi chifukwa anakwiya kwambiri ndi kutengedwa kwa ana awo aamuna ndi aakazi. Koma Davide anakhulupirira Yehova Mulungu wake ndipo anapeza mphamvu.+