10 Choncho ndinapita nʼkukamupha+ chifukwa ndinadziwa kuti sakhalanso ndi moyo popeza anali atagwa komanso atavulala kwambiri. Kenako ndinatenga chipewa chachifumu chimene chinali kumutu kwake ndi khoza lomwe anavala pamkono ndipo ndabwera nazo kwa inu mbuyanga.”