-
2 Samueli 3:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Abineri atamva mawu a Isi-bosetiwa anakwiya kwambiri ndipo anati: “Kodi ndine galu wopanda pake wa Yuda? Ineyo ndakhala ndikusonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu a nyumba ya Sauli bambo ako, azichimwene ake komanso anzake ndipo sindinakupereke mʼmanja mwa Davide. Koma lero ukundiimba mlandu pa zimene ndinalakwitsa zokhudza mkazi.
-