10 Iweyo, ana ako aamuna ndi antchito ako, muzimulimira minda yake ndiponso kumukololera kuti anthu amʼnyumba ya mdzukulu wa mbuye wako azikhala ndi chakudya. Koma Mefiboseti, mdzukulu wa mbuye wako, azidya patebulo langa nthawi zonse.”+
Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi antchito 20.+