5 Atatero, Yehonadabu anamuuza kuti: “Ugone pabedi lako ndipo unamizire kudwala. Bambo ako akabwera kudzakuona, udzawauze kuti, ‘Ndikupempha kuti mchemwali wanga Tamara abwere kudzandipatsa chakudya. Akadzandikonzera chakudya, ine ndikuona, ndidzadya kuchokera mʼmanja mwake.’”