20 Zitatero, mchimwene wake Abisalomu+ anamufunsa kuti: “Kodi unali ndi mchimwene wako Aminoni? Ingokhala chete mchemwali wanga. Ameneyu ndi mchimwene wako.+ Usadandaule nazo kwambiri, ingozisiya.” Ndiyeno Tamara ankangokhala kunyumba kwa mchimwene wake Abisalomu ndipo sankacheza ndi aliyense.