2 Choncho Yowabu anatumiza anthu ku Tekowa+ kuti akatenge mayi wochenjera. Atabwera naye, anamuuza kuti: “Chonde ukhale ngati munthu amene akulira maliro, uvale zovala zolirira maliro komanso usadzole mafuta.+ Ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira maliro kwa nthawi yaitali.