2 Abisalomu ankadzuka mʼmawa kwambiri nʼkukaima mʼmbali mwa msewu wopita kugeti la mzinda.+ Ndiyeno munthu aliyense akafika ndi mlandu woti uweruzidwe ndi mfumu,+ Abisalomu ankamuitana nʼkumufunsa kuti: “Wachokera mzinda uti?” Munthuyo ankamuuza fuko la Isiraeli limene wachokera.