14 Nthawi yomweyo, Davide anauza atumiki ake onse amene anali naye ku Yerusalemu kuti: “Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithawe,+ chifukwa palibe amene angapulumuke mʼmanja mwa Abisalomu. Fulumirani! Chifukwa akhoza kutipeza nʼkutigonjetsa kenako nʼkupha anthu onse amumzindawu ndi lupanga!”+