8 Husai ananenanso kuti: “Inu mukudziwa bwino kuti bambo anu ndi amuna amene ali nawo, onse ndi amphamvu+ ndipo mitima ikuwapweteka ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa mʼtchire.+ Komanso bambo anu ndi munthu wodziwa nkhondo+ ndipo sangagone kumene kuli anthu.