3 Koma anthuwo anati: “Ayi musapite,+ chifukwa ngati tingakathawe, sakalimbana ndi ife. Ndipo ngati hafu ya ife ingakafe, sakakhutira nazo chifukwa inuyo ndinu wofunika kuposa asilikali 10,000.+ Choncho zingakhale bwino kuti muzitithandiza muli mumzinda momʼmuno.”