9 Kenako Abisalomu anakumana ndi atumiki a Davide. Abisalomu anali atakwera nyulu, ndipo nyuluyo inadutsa pansi pa ziyangoyango za nthambi za mtengo waukulu kwambiri. Choncho mutu wa Abisalomu unakola muziyangoyangozo koma nyulu imene anakwerapoyo inadutsa moti inamusiya akulendewera.