33 Zimenezi zinakhumudwitsa kwambiri mfumu ndipo inapita mʼchipinda chapadenga chapageti nʼkuyamba kulira, uku ikuyendayenda. Mfumu inkanena kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ineyo mʼmalo mwa iwe, Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+