10 Koma Amasa sanali tcheru ndi lupanga limene linali mʼmanja mwa Yowabu. Choncho Yowabuyo anamubaya nalo mʼmimba+ ndipo matumbo ake anakhuthukira pansi. Anangomubaya kamodzi nʼkuferatu, sanachite kumubaya kawiri. Kenako Yowabu ndi mchimwene wake Abisai anapitiriza kusaka Sheba mwana wa Bikiri.