21 Nkhani siili choncho. Koma munthu wochokera kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Sheba+ mwana wa Bikiri, waukira Mfumu Davide. Inu mukangotipatsa munthu ameneyu, ine ndiusiya mzindawu.” Mayiyo anauza Yowabu kuti: “Tikuponyerani mutu wake kuchokera pamwamba pa mpanda!”