8 Choncho mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, amene anali ana awiri aamuna a Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya, amene Rizipayo anaberekera Sauli. Anatenganso ana aamuna 5 a Mikala,+ mwana wamkazi wa Sauli, amene anaberekera Adiriyeli,+ mwana wa Barizilai wa ku Mehola.