10 Kenako Rizipa+ mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli nʼkuchiyala pamwala kuti azikhalapo, kuyambira kumayambiriro kwa nthawi yokolola mpaka pamene mvula inagwera pamitemboyo. Iye sanalole mbalame zamumlengalenga kutera pamitemboyo masana, ndipo usiku sanalole zilombo zakutchire kuyandikirapo.