20 Benaya+ mwana wa Yehoyada, anali munthu wolimba mtima ndipo anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu komanso analowa mʼchitsime chopanda madzi pa tsiku lomwe kunagwa sinowo nʼkupha mkango umene unali mʼchitsimemo.+