16 Mngelo atatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha mliriwo,+ choncho anauza mngelo amene ankapha anthuyo kuti: “Basi! Bweza dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehovayo anali pafupi ndi malo opunthira mbewu a Arauna+ wa Chiyebusi.+