9 Kenako Adoniya anapereka nsembe+ za nkhosa, ngʼombe komanso ana a ngʼombe onenepa pafupi ndi mwala wa Zoheleti womwe uli pafupi ndi Eni-rogeli. Anaitana azichimwene ake onse omwe anali ana a mfumu komanso amuna onse a mu Yuda omwe anali atumiki a mfumu.