25 Chifukwatu lero wapita kukapereka nsembe+ zambiri za ngʼombe zamphongo, nyama zonenepa ndi nkhosa. Waitananso ana onse a mfumu, atsogoleri a asilikali komanso wansembe Abiyatara.+ Moti panopa ali kumeneko ndipo akudya ndi kumwa naye nʼkumanena kuti, ‘Mfumu Adoniya ikhale ndi moyo wautali!’