3 Uzimvera Yehova Mulungu wako poyenda mʼnjira zake komanso posunga malamulo ake, ziweruzo zake ndiponso zikumbutso zake mogwirizana ndi mmene anazilembera mʼChilamulo cha Mose.+ Ukatero zinthu zidzakuyendera bwino pa zonse zimene ungachite ndiponso kulikonse kumene ungapite.