22 Mfumu Solomo inayankha mayi akewo kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukupempha kuti Abisagi wa ku Sunemu akhale mkazi wa Adoniya? Ndiyetu mumupempherenso ufumu,+ popeza iye ndi mkulu wanga+ ndipo wansembe Abiyatara ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ ali kumbali yake.”