26 Mfumuyo inauza wansembe Abiyatara+ kuti: “Pita kuminda yako ku Anatoti.+ Umayenera kufa, koma lero sindikupha chifukwa unanyamula Likasa la Yehova Ambuye Wamkulu Koposa pamaso pa Davide bambo anga+ ndiponso chifukwa chakuti unavutika limodzi ndi bambo anga pa nthawi yonse imene ankavutika.”+