3 Solomo anachita mgwirizano wa ukwati ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anakwatira mwana wamkazi wa Farao+ nʼkubwera naye mu Mzinda wa Davide,+ kuti azikhala kaye kumeneko mpaka iye atamaliza kumanga nyumba yake,+ nyumba ya Yehova+ ndiponso mpanda wa Yerusalemu.+