13 Mwana wa Geberi ankayangʼanira ku Ramoti-giliyadi+ (dera lake linali midzi ingʼonoingʼono ya Yairi+ mwana wa Manase, yomwe ili ku Giliyadi.+ Analinso ndi chigawo cha Arigobi,+ chomwe chili ku Basana.+ Kunali mizinda ikuluikulu 60 yokhala ndi mipanda komanso zotchingira zakopa).