9 Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni nʼkupita nayo kunyanja, ndipo ndidzaimanga pamodzi ngati phaka nʼkuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze. Kenako akaimasula ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Malipiro ake mudzandipatsa chakudya cha banja langa.”+