11 Ndipo Solomo anapereka kwa Hiramu tirigu wokwana miyezo 20,000 ya kori, kuti chikhale chakudya cha banja lake, ndiponso mafuta a maolivi oyenga bwino okwana miyezo 20 ya kori. Zinthu zimenezi ndi zomwe Solomo ankapereka kwa Hiramu chaka chilichonse.+