2 Kenako anamanga nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ Nyumbayi inali mikono 100 mulitali, mikono 50 mulifupi ndiponso mikono 30 kupita mʼmwamba. Anaimanga pamwamba pa nsanamira za mtengo wa mkungudza.+ Nsanamirazo zinali mʼmizere 4 ndipo pamwamba pake anaikapo mitengo ya mkungudza.