8 Kenako Solomo anamanga nyumba yake yokhalamo chapatali ndi nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu.+ Kamangidwe ka nyumbayi kanali kofanana ndi ka nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu. Solomo anamanganso nyumba ina yofanana ndi Bwaloli ndipo anamangira mwana wamkazi wa Farao amene iye anamʼkwatira.+