25 Thankiyo anaikhazika pangʼombe zamphongo 12.+ Ngʼombe zitatu zinayangʼana kumpoto, zitatu zinayangʼana kumadzulo, zitatu zinayangʼana kumʼmwera ndipo zitatu zinayangʼana kumʼmawa. Thankiyo inali pamwamba pa ngʼombezo ndipo mbuyo zonse za ngʼombezo zinaloza pakati.