50 mabeseni, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa, makapu+ ndiponso zopalira moto.+ Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso molowa miyendo ya zitseko za chipinda chamkati,+ kutanthauza Malo Oyera Koposa ndiponso molowa miyendo ya zitseko za nyumbayo.+ Zonsezi zinali zagolide.