48 nʼkubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ mʼdziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayangʼana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, mzinda umene mwasankha komanso nyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+