12 Mfumuyo inagwiritsa ntchito matabwa a mʼbawawo popanga zochirikizira nyumba ya Yehova komanso nyumba ya mfumu. Inagwiritsanso ntchito matabwawo kupanga azeze ndi zoimbira za zingwe za oimba.+ Matabwa a mʼbawa otere sanabwereponso kapena kuoneka mpaka lero.