38 Ukamvera malamulo anga onse, kuyenda mʼnjira zanga ndiponso kuchita zoyenera pamaso panga posunga malamulo anga ngati mmene anachitira mtumiki wanga Davide,+ inenso ndidzakhala nawe. Ana ako adzalamulira kwa nthawi yaitali mofanana ndi ana a Davide,+ ndipo ndidzakupatsa Isiraeli.