32 Yerobowamu anakhazikitsa chikondwerero chofanana ndi cha ku Yuda pa tsiku la 15 la mwezi wa 8.+ Paguwa la nsembe limene analimanga ku Beteli,+ anaperekapo nsembe kwa ana a ngʼombe amene anawapanga aja ndipo ku Beteliko anasankha ansembe kuti azitumikira mʼmalo okwezeka amene anapanga.