10 Pa chifukwa chimenechi, ndikubweretsa tsoka panyumba ya Yerobowamu ndipo ndidzapha mwamuna aliyense wamʼnyumba ya Yerobowamu, ngakhale ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli. Komanso ndidzaseseratu nyumba ya Yerobowamu+ ngati mmene munthu amasesera ndowe mpaka zonse zitachoka.