21 Pa nthawiyi, Rehobowamu mwana wa Solomo anali mfumu ku Yuda. Rehobowamu anali ndi zaka 41 pamene ankayamba kulamulira, ndipo analamulira kwa zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anasankha+ pa mafuko onse a Isiraeli kuti aikeko dzina lake.+ Mayi ake anali Naama, mbadwa ya Amoni.+