4 Ndipo iyeyo analowa mʼchipululu nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake nʼkukhala pansi pake. Ndiyeno anapempha kuti afe ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova,+ chifukwa siine woposa makolo anga.”