10 Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+ koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga,+ moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+