43 Yehosafati anapitiriza kuyenda mʼnjira zonse za Asa,+ bambo ake. Sanasiye kuyenda mʼnjirazo ndipo anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Koma sanachotse malo okwezeka ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi komanso nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+