17 Kenako mfumu ya Asuri inatuma Tatani, Rabisarisi ndi Rabisake kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu.+ Inawatumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali. Iwo anakaima pafupi ndi ngalande yochokera kudziwe lakumtunda, pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+