13 “Pitani mukafunse kwa Yehova mʼmalo mwa ineyo, anthuwa ndiponso mʼmalo mwa Ayuda onse. Mukafunse zokhudza mawu a mʼbuku limene lapezekali, chifukwa Yehova watikwiyira kwambiri,+ popeza makolo athu sanamvere mawu a mʼbukuli. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.”