17 Kenako iye anati: “Kodi chipilala chimene ndikuchiona apocho nʼcha chiyani?” Amuna amumzindawo anamuyankha kuti: “Ndi manda a munthu wa Mulungu woona amene anachokera ku Yuda,+ yemwe analosera zinthu zotsutsa guwa lansembe la ku Beteli, zimene mwachitazi.”