24 Yosiya anachotsanso anthu olankhula ndi mizimu, olosera zamʼtsogolo,+ zifaniziro za aterafi,+ mafano onyansa ndi zonyansa zonse zimene zinali ku Yuda ndi ku Yerusalemu, kuti atsatire mawu a Chilamulo+ amene analembedwa mʼbuku lomwe wansembe Hilikiya analipeza mʼnyumba ya Yehova.+