13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha mʼnyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapanga kuti zikhale za mʼkachisi wa Yehova.+ Zimenezi zinachitika mogwirizana ndi zimene Yehova analosera.