25 Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse.+ Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+