17 Chipilala chilichonse chinali chachitali mikono 18+ ndipo mutu wake unali wakopa. Mutuwo unali wautali mikono itatu ndipo maukonde ndi makangaza amene anazungulira mutuwo, onse anali akopa.+ Chipilala chachiwiri ndi maukonde ake chinalinso chofanana ndi choyambacho.